Skip to main content

Chichewa - The Book of Joshua

Page 1

Yoswa MUTU 1 1 Ndipo kunali atafa Mose mtumiki wa Yehova, Yehova ananena ndi Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose, ndi kuti, 2 Mose mtumiki wanga wafa; tsono nyamuka, nuoloke Yordano uyu, iwe ndi anthu awa onse, kulowa m’dziko limene ndiwapatsa ana a Israyeli. 3 Malo onse amene mapazi anu adzapondapo ndakupatsani inu, monga ndinanena kwa Mose. + 4 Kuyambira kuchipululu ndi ku Lebanoni + mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate, + dziko lonse la Ahiti, + mpaka ku Nyanja Yaikulu ya kulowera dzuwa, + ndiye malire anu. 5 Palibe munthu adzaima pamaso pako masiku onse a moyo wako; monga ndinakhala ndi Mose, momwemo ndidzakhala ndi iwe; sindidzakusiya, sindidzakutaya. 6 Khala wamphamvu, nulimbike mtima, pakuti udzagawira anthu awa dzikolo, limene ndinalumbirira makolo ao kuti ndidzawapatsa, likhale colowa cao. 7 Koma khala wamphamvu ndi wolimba mtima ndithu, kuti usamalire kuchita monga mwa chilamulo chonse chimene Mose mtumiki wanga anakulamulirani; 8 Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma uzilingiriramo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; 9 Kodi sindinakulamulira iwe? Khala wamphamvu, limbika mtima; usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kuli konse umukako. 10 Pamenepo Yoswa analamulira akapitawo a anthu, kuti, 11 Pita pakati pa khamulo, nuuze anthu, ndi kuti, Konzekerani inu zakudya; + pakuti pasanathe masiku atatu mudzawoloka Yorodano ameneyu kuti mulowe m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani kuti likhale lanu lanu. 12 Ndipo Yoswa ananena kwa Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu ya fuko la Manase, kuti, 13 Kumbukirani mawu amene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani, kuti, Yehova Mulungu wanu wakupumulitsani, nakupatsani dziko ili. 14 Akazi anu, ana anu aang’ono, ndi ng’ombe zanu adzakhala m’dziko limene Mose anakupatsani tsidya lija la Yordano; koma inu mudzaoloka pamaso pa abale anu okonzeka, amuna onse amphamvu ndi olimba mtima, ndi kuwathandiza; 15 kufikira Yehova atapumulitsa abale anu, monga anakupatsani inu, kuti iwonso alandire dziko limene Yehova Mulungu wanu awapatsa; pamenepo mudzabwerera ku dziko lanu lanu, ndi kulidya, limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani tsidya lija la Yordano, kotulukira dzuwa. 16 Ndipo anayankha Yoswa, nati, Zonse mwatilamulira tidzachita, ndi kuli konse mudzatitumiza ife tidzamuka. 17 Monga tinamvera Mose m’zonse, momwemo tidzamvera inu; koma Yehova Mulungu wanu akhale ndi inu, monga anali ndi Mose. + 18 Aliyense wopandukira + malamulo anu, + osamvera mawu anu + m’zonse zimene munamulamula, + aziphedwa.

MUTU 2 1 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anatumiza amuna awiri okazonda mtseri kucokera ku Shitimu, nati, Mukani, muone dziko, ndilo Yeriko. Ndipo anamuka, nalowa m'nyumba ya mkazi wadama, dzina lake Rahabi, nagona kumeneko. 2 Ndipo anauza mfumu ya Yeriko, kuti, Taonani, analowa muno usiku uno amuna a ana a Israyeli kudzazonda dziko. 3 Ndipo mfumu ya Yeriko inatumiza uthenga kwa Rahabi, ndi kuti, Tulutsa amuna amene afika kwa iwe, amene alowa m’nyumba mwako, pakuti abwera kudzazonda dziko lonse. 4 Ndipo mkaziyo anatenga amuna awiri aja, nawabisa, nati, Anadza kwa ine amuna, koma sindinadziwa kumene akuchokera; 5 Ndipo kunali, potseka pacipata, kutada, amunawo anaturuka; kumene ananka amunawo sindikudziŵa; pakuti mudzawapeza. 6 Koma iye anawakwera pamwamba pa tsindwi la nyumba, nawabisa ndi mapesi a fulakesi, amene anawayala patsindwi. 7 Ndipo amunawo anawalondola panjira ya ku Yorodano yopita ku madooko; 8 Ndipo asanagone, iye anakwera kwa iwo padenga; 9 Ndipo iye anati kwa amunawo, Ndidziŵa kuti Yehova wakupatsani dzikoli, ndi kuti mantha anu atigwera, ndi kuti onse okhala m’dziko akomoka chifukwa cha inu. 10 Pakuti tinamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a m’Nyanja Yofiira pamaso panu, muja munatuluka mu Igupto; ndi zimene munachitira mafumu awiri a Aamori okhala kutsidya lija la Yordano, Sihoni ndi Ogi, amene munawaononga konse. 11 Ndipo titangomva zimenezi, mitima yathu inasungunuka, + ndipo palibe munthu amene anakhala wolimba mtima chifukwa cha inu, + pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wakumwamba ndi padziko lapansi. 12 Tsopano, ndikukupemphani, mulumbirire kwa Yehova + kuti, popeza ndakukomerani mtima, + inunso mudzachitira banja la atate wanga kukoma mtima + ndi kundipatsa chizindikiro choona. 13 ndi kuti mupulumutse atate wanga, ndi amayi wanga, ndi abale anga, ndi alongo anga, ndi zonse ali nazo, ndi kupulumutsa moyo wathu kuimfa. 14 Ndipo amunawo anamyankha iye, Moyo wathu m’malo mwanu, mukapanda kunena za ntchito yathu iyi. Ndipo kudzali, pamene Yehova watipatsa dzikolo, tidzakucitira cifundo ndi coonadi. 15 Pamenepo anawatsitsa pa zenera ndi chingwe, pakuti nyumba yake inali pa linga la mudzi, ndipo iye anakhala pamwamba pa linga. 16 Ndipo iye anati kwa iwo, Pitani inu kuphiri, kuti olondola angakumane nanu; ndipo mubisale komweko masiku atatu, mpaka abwerere olondolawo; 17 Ndipo amunawo anati kwa iye, Tidzakhala opanda cholakwa pa lumbiro lako limene watilumbiritsa. 18 Taona, tikadzalowa m’dzikolo, uzimanga chingwe chofiirachi pa zenera limene watitsitsirapo, ndipo ubwere nawo kunyumba kwako atate wako, ndi amako, ndi abale ako, ndi onse a m’nyumba ya atate wako.


Turn static files into dynamic content formats.

Create a flipbook