1 Mafumu MUTU 1 1 Ndipo mfumu Davide anali wokalamba, wa zaka zambiri; ndipo adamfunda iye ndi zobvala, koma sanatenthedwa. 2 Pamenepo atumiki ake anati kwa iye, Afunikire mbuyanga mfumu namwali, aimirire pamaso pa mfumu, amsunge, agone pa chifuwa chanu, kuti mbuye wanga mfumu mutenthedwe. 3 Choncho anafunafuna namwali wokongola + m’madera onse a Isiraeli, ndipo anapeza Abisagi wa ku Sunamu n’kupita naye kwa mfumu. 4 Ndipo namwaliyo anali wokongola ndithu, nasamalira mfumu, namtumikira; koma mfumu sinamdziwa iye. + 5 Pamenepo Adoniya + mwana wa Hagiti anadzikuza + n’kunena kuti: “Ine ndidzakhala mfumu.” + Choncho anadzikonzera magaleta ankhondo ndi apakavalo ndi amuna 50 othamanga pamaso pake. 6 Ndipo atate wake sanamukwiyitsa nthawi iri yonse ndi kuti, Watero chifukwa ninji? ndipo iyenso anali munthu wokongola ndithu; ndi amake anam’bala pambuyo pa Abisalomu. 7 Anakambirana ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi Abiyatara wansembe, ndipo iwo anatsatira Adoniya anamuthandiza. 8 Koma Zadoki wansembe, + Benaya + mwana wa Yehoyada, + mneneri Natani, + Simeyi, + Rei, + ndi amuna amphamvu + amene anali a Davide, sanagwirizane ndi Adoniya. + 9 Adoniya anapha + nkhosa ndi ng’ombe + ndi ng’ombe zonenepa pafupi ndi mwala wa Zoheleti + umene uli pafupi ndi Enirogeli, + ndipo anaitana abale ake onse, + ana a mfumu, + ndi amuna onse a ku Yuda, atumiki a mfumu. 10 Koma Natani mneneri, ndi Benaya, ndi amuna amphamvu, ndi Solomo mbale wake, sanaitana. + 11 Choncho Natani anauza Bati-seba + mayi ake a Solomo kuti: “Kodi sunamve kuti Adoniya mwana wa Hagiti wayamba kulamulira, koma mbuye wathu Davide sakudziwa zimenezi? 12 Tsopano tiyeni ndikupangire uphungu, kuti upulumutse moyo wako ndi moyo wa mwana wako Solomo. + 13 Pita ukalowe kwa Mfumu Davide, + ndi kukamuuza kuti, ‘Kodi inu mbuyanga mfumu, simunalumbirira mdzakazi wanu kuti, ‘Ndithu Solomo mwana wako adzakhala mfumu pambuyo panga, ndipo iye adzakhala pampando wanga wachifumu? Nanga Adoniya ayamba bwanji kukhala mfumu? 14 Taona, uli chilankhulire ndi mfumu, inenso ndidzalowa pambuyo pako, ndi kutsimikizira mau ako. 15 Ndipo Bati-seba analowa kwa mfumu m’chipinda chodyera, ndipo mfumuyo inali yokalamba ndithu; ndi Abisagi Msunemu anatumikira mfumu. 16 Ndipo Bati-seba anagwada, nawerama pamaso pa mfumu. Ndipo mfumu inati, Mufuna ciani? 17 Ndipo iye anati kwa iye, Mbuye wanga, munalumbirira mdzakazi wanu pa Yehova Mulungu wanu, kuti, Zoonadi Solomo mwana wako adzakhala mfumu pambuyo panga, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu. 18 Tsopano taonani, Adoniya wayamba kulamulira. ndipo tsopano, mbuye wanga mfumu, simudziwa;
19 Wapha ng’ombe, ng’ombe zonenepa, ndi nkhosa zambiri, naitana ana onse a mfumu, ndi Abiyatara wansembe, ndi Yowabu, kazembe wa nkhondo; 20 Ndipo inu, mbuye wanga mfumu, maso a Aisrayeli onse ali pa inu, kuti muwauze amene adzakhala pa mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu pambuyo pake. 21 Apo ayi, mbuye wanga mfumu akagona ndi makolo ake, ine ndi mwana wanga Solomo tidzayesedwa olakwa. 22 Ndipo, taonani, ali chilankhulire ndi mfumu, mneneri Natani analowanso. 23 Ndipo anauza mfumu, kuti, Onani Natani mneneriyo. Ndipo analowa pamaso pa mfumu, nawerama pamaso pa mfumu nkhope yake pansi. 24 Ndiyeno Natani anati: “Mbuye wanga mfumu, kodi munati, ‘Adoniya ndiye adzakhala mfumu pambuyo panga, ndipo iye adzakhala pampando wanga wachifumu? 25 Pakuti lero watsikira kukapha ng’ombe, ng’ombe zonenepa, ndi nkhosa zambiri, naitana ana onse a mfumu, ndi akazembe ankhondo, ndi Abiyatara wansembe; ndipo taonani, akudya ndi kumwa pamaso pace, nati, Mfumu Adoniya ikhale ndi moyo. 26 Koma ine, inenso mtumiki wanu, ndi Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Solomo mtumiki wanu, sanatiitane. 27 Kodi ichi chachitidwa ndi mbuyanga mfumu, ndipo simunachidziwitse ine kapolo wanu, amene adzakhala pampando wachifumu wa mbuye wanga mfumu pambuyo pake? 28 Pamenepo mfumu Davide anayankha, nati, Ndiitanireni Bati-seba. Ndipo iye analowa pamaso pa mfumu, naima pamaso pa mfumu. 29 Ndipo mfumu inalumbira, ndi kuti, Pali Yehova, amene anaombola moyo wanga m’masautso onse; 30 monga ndinalumbirira kwa Yehova Mulungu wa Israyeli, ndi kuti, Zedi Solomo mwana wako adzakhala mfumu pambuyo panga, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu m’malo mwanga; momwemonso ndidzachita lero. 31 Pamenepo Bati-seba anawerama ndi nkhope yake pansi, nagwadira mfumu, nati, Mbuye wanga mfumu Davide akhale ndi moyo kosatha. 32 Ndipo mfumu Davide anati, Ndiitanireni Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada. Ndipo anadza pamaso pa mfumu. 33 Mfumuyo inawauzanso kuti: “Tengani atumiki a mbuye wanu, + ndipo mukwere naye Solomo mwana wanga pa nyuru yanga + ndi kutsika naye ku Gihoni. 34 Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri amdzoze kumeneko kukhala mfumu ya Israyeli; 35 Pamenepo mukwere pambuyo pake, kuti adze nakhala pa mpando wanga wachifumu; pakuti adzakhala mfumu m’malo mwanga; 36 Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu, nati, Amen, ateronso Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu. 37 Monga Yehova anakhala ndi mbuyanga mfumu, momwemo akhale ndi Solomo, nakuze mpando wachifumu wake ukuposa mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu Davide. 38 Pamenepo Zadoki wansembe, + mneneri Natani, + Benaya + mwana wa Yehoyada, + Akereti + ndi Apeleti + anatsika, n’kukweza Solomo pa nyuru ya Mfumu Davide n’kupita naye ku Gihoni.